2 Samuel 13:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku lina Yonadabu adafunsa Aminoni kuti, “Kodi iwe, mwana wa mfumu, chifukwa chiyani umaoneka woonda m'maŵa masiku onse? Bwanji osandiwuza ine?” Aminoni adamuyankha kuti, “Ine ndikukonda Tamara, mlongo wa mkulu wanga Abisalomu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nanena naye, Iwe mwana wa mfumu, uonderanji tsiku ndi tsiku? Sungandiuze kodi? Ndipo Aminoni anati kwa iye, Ndikonda Tamara, mlongo wa mbale wanga Abisalomu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anafunsa Amnoni, “Nʼchifukwa chiyani iwe mwana wa mfumu, umaoneka wowonda mmawa uliwonse? Bwanji wosandiwuza?” Amnoni anamuyankha kuti, “Ine ndamukonda Tamara, mlongo wa mʼbale wanga Abisalomu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nanena naye, Iwe mwana wa mfumu, uonderanji tsiku ndi tsiku? Sungandiuze kodi? Ndipo Amnoni anati kwa iye, Ndikonda Tamara, mlongo wa mbale wanga Abisalomu.