2 Samuel 13:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Yonadabu adamuuza kuti, “Kagone pabedi pako, ndipo uchite ngati wadwala. Bambo wako akafika kuti adzakuwone, umuuze kuti, ‘Mloleni Tamara, mlongo wanga, abwere andikonzere chakudya kuti ndidye. Adzandikonzere chakudyacho konkuno, ine ndikupenya, kuti ndichiwone, ndipo ndidzadyere m'manja mwake.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yonadabu ananena naye, Ugone pa kama wako ndi kudzikokomera ulikudwala; ndipo pamene atate wako akadzakuona unene naye, Mulole mlongo wanga Tamara abwere kundipatsa kudya, nakonzere chakudyacho pamaso panga kuti ndichione ndi kuchidya cha m'manja mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehonadabu anati, “Pita ukagone ndipo unamizire kudwala. Abambo ako akabwera kudzakuona, udzati kwa iwo, Ine ndikufuna mlongo wanga Tamara abwere kuti adzandikonzere chakudya kuti ndidye. Adzandikonzere chakudyacho ine ndikumuona ndi kudya chili mʼmanja mwake.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Jonadabu ananena naye, Ugone pa kama wako ndi kudzikokomeza ulikudwala; ndipo pamene atate wako akadzakuona unene naye, Mulole mlongo wanga Tamara abwere kundipatsa kudya, nakonzere cakudyaco pamaso panga kuti ndicione ndi kucidya ca m'manja mwace.