2 Samuel 14:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo mfumu idati, “Ngati wina aliyense akunenerani kanthu kena kalikonse, mubwere naye kwa ine, ndipo sadzakuvutitsaninso.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu inati, Ubwere naye kwa ine aliyense wakunena kanthu ndi iwe, ndipo iyeyo sadzakukhudzanso.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu inayankha kuti, “Ngati wina aliyense anene kanthu kwa iwe, umubweretse kwa ine, ndipo sadzakuvutitsanso.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu inati, Ubwere naye kwa ine ali yense wakunena kanthu ndi iwe, ndipo iyeyo sadzakukhudzanso.