2 Samuel 14:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mkazi uja adanena kuti, “Chonde, amfumu mupemphe kwa Chauta Mulungu wanu, kuti wolipsira imfa ija asaphenso wina, kuti choncho mwana wanga asaonongeke.” Davide adati, “Pali Chauta wamoyo, mwana wanu sadzapwetekedwa mpang'ono pomwe.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati iye, Mfumu mukumbukire Yehova Mulungu wanu kuti wolipsa mwazi asaonjeze kuononga, kuti angaononge mwana wanga. Niti iyo, Pali Yehova, palibe tsitsi limodzi la mwana wako lidzagwa pansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mkaziyo anati, “Mfumu ipemphe kwa Yehova Mulungu wake kuti aletse wobwezera imfa asaphenso wina kuti mwana wanga asawonongedwe.” Mfumu inati, “Pali Yehova wamoyo ngakhale tsitsi limodzi la pamutu pa mwana wako silidzathotholedwa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati iye, Mfumu mukumbukile Yehova Mulungu wanu kuti wolipsa mwazi asaonjeze kuononga, kuti angaononge mwana wanga. Niti iyo, Pali Yehova, palibe tsitsi limodzi la mwana wako lidzagwa pansi.