2 Samuel 14:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo mkazi uja adafunsa kuti, “Chifukwa chiyani nanga mwaganiza zoŵachita zinthu zotere anthu a Mulungu? Chifukwatu pochita zimenezi inu amfumu mwadziimba mlandu nokha, malinga nkuti simudaitanitse wopirikitsidwa uja kuti abwererenso kwao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mkaziyo anati, Chifukwa ninjinso munalingalira chinthu chotere pa anthu a Mulungu? Pakuti pakulankhula mau awa mfumu ikunga wopalamula, popeza mfumu siitumiza okamtenganso woingidwa wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mkaziyo anati, “Nʼchiyani tsono chimene mwaganiza kuchitira zimenezi anthu a Mulungu? Pamene mfumu yanena izi, kodi sikudzitsutsa yokha, pakuti mfumu sinayitanitse mwana amene anamupirikitsa?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mkaziyo anati, Cifukwa ninjinso munalingalira cinthu cotere pa anthu a Mulungu? pakuti pakulankhula mau awa mfumu ikunga woparamula, popeza mfumu siitumiza okamtenganso woingidwa wace.