2 Samuel 14:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndimaganiza kuti inu amfumu mutazimva, mudzandipulumutsa kwa munthu amene afuna kundiwononga ine pamodzi ndi mwana wanga, potero nkutichotsa pa kadziko kathu kamene adatipatsa Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti mfumu idzamvera ndi kupulumutsa mdzakazi wake m'dzanja la munthu wakufuna kundiononga ine pamodzi ndi mwana wanga, kutichotsa ku cholowa cha Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwina mfumu idzavomereza kupulumutsa mdzakazi wake mʼdzanja la munthu amene akufuna kupha ine pamodzi ndi mwana wanga kutichotsa pa cholowa chimene Mulungu anatipatsa.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti mfumu idzamvera ndi kupulumutsa mdzakazi wace m'dzanja la munthu wakufuna kundiononga ine pamodzi ndi mwana wanga, kuticotsa ku colowa ca Mulungu.