2 Samuel 14:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho ine mdzakazi wanu ndidaaganiza kuti mau anu mbuyanga mfumu adzandipulumutsa, poti inu muli ngati mngelo wa Mulungu, podziŵa zabwino ndi zoipa. Chauta Mulungu wanu akhale nanu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mdzakazi wanu ndinati, Mau a mbuye wanga mfumu akhale opumulitsa; mbuye wanga mfumu ali ngati mthenga wa Mulungu, kuzindikira zabwino ndi zoipa; ndipo Yehova Mulungu wanu akhale nanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndipo tsopano mtumiki wanu akuti, ‘Lolani mawu a mbuye wanga mfumu abweretse mpumulo kwa ine, pakuti mbuye wanga mfumu ali ngati mngelo wa Mulungu pozindikira chabwino ndi choyipa. Yehova Mulungu wanu akhale nanu.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mdzakazi wanu ndinati, Mau a mbuye wanga mfumu akhale opumulitsa; mbuye wanga mfumu ali ngati mthenga wa Mulungu, kuzindikira zabwino ndi zoipa; ndipo Yehova Mulungu wanu akhale nanu.