2 Samuel 14:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mfumuyo idafunsa kuti, “Kodi zimenezi Yowabu sakuzidziŵa?” Mkaziyo adayankha kuti, “Pali inu nomwe, mbuyanga mfumu, palibe munthu amene angathe kupewa kuyankha chilichonse chimene inu mwafunsa. Kunena zoona, mtumiki wanu Yowabu ndiye amene adandiwuza kuti ndichite zimenezi. Iyeyo ndiye adandiwuza ine mdzakazi wanu mau onseŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumuyo inati, Kodi Yowabu adziwana ndi iwe mwa izi zonse? Mkaziyo nayankha nati, Pali moyo wanu mbuye wanga mfumu, palibe kulewa ku dzanja lamanja, kapena kulamanzere kwa zonse mudazinena mbuye wanga mfumu; pakuti mnyamata wanu Yowabu ndiye anandiuza, naika mau onse awa m'kamwa mwa mdzakazi wanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu inafunsa kuti, “Kodi zimenezi sukuchita motsogozedwa ndi Yowabu?” Mkaziyo anayankha kuti, “Pali inu wamoyo, mbuye wanga mfumu, palibe munthu angakhotere kumanja kapena kumanzere pa chilichonse chimene mbuye wanga mfumu mwanena. Inde, ndi mtumiki wanu Yowabu amene wandilangiza ine kuchita zimenezi ndipo ndi amene anandipatsa mawu onsewa woti ine mtumiki wanu ndiyankhule.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumuyo inati, Kodi Yoabu adziwana ndi iwe mwa izi zonse? Mkaziyo nayankha nati, Pali moyo wanu mbuye wanga mfumu, palibe kulewa ku dzanja lamanja, kapena kulamanzere kwa zonse mudazinena mbuye wanga mfumu; pakuti mnyamata wanu Yoabu ndiye anandiuza, naika mau onse awa m'kamwa mwa mdzakazi wanu.