2 Samuel 14:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mtumiki wanu Yowabu adachita zimenezi kuti asinthe mayendedwe ake a zinthu. Koma inu mbuyanga muli ndi nzeru zonga za mngelo wa Mulungu, mutha kudziŵa zinthu zonse za pa dziko lapansi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mnyamata wanu Yowabu anachita chinthu ichi kuti asandulize mamvekedwe a mlanduwo. Ndipo mbuye wanga ali wanzeru, monga ndi nzeru ya mthenga wa Mulungu, kudziwa zonse zili m'dziko lapansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mtumiki wanu Yowabu anachita zimenezi kuti asinthe mmene zinthu zilili lero. Mbuye wanga muli ndi nzeru ngati za mngelo wa Mulungu. Mumadziwa zonse zimene zikuchitika mʼdziko.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mnyamata wanu Yoabu anacita cinthu ici kuti asandulize mamvekedwe a mranduwo. Ndipo mbuye wanga ali wanzeru, monga ndi nzeru ya mthenga wa Mulungu, kudziwa zonse ziri m'dziko lapansi.