2 Samuel 14:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake mfumu idauza Yowabu kuti, “Chabwino tsono, ndavomera kuti zimenezi zichitike. Pita, kamtenge mnyamata uja Abisalomu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumuyo inanena ndi Yowabu, Taonanitu, ndachita chinthu ichi; chifukwa chake, pita nubwere nayenso mnyamatayo Abisalomu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu inati kwa Yowabu, “Chabwino, ine ndichita zimenezi. Pita kamutenge Abisalomuyo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumuyo inanena ndi Yoabu, Taonatu, ndacita cinthu ici; cifukwa cace, pita nubwere nayenso mnyamatayo Abisalomu.