2 Samuel 14:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komabe mfumu idati, “Akhale payekha m'nyumba yakeyake. Asabwere pamaso panga.” Motero Abisalomu adakhala pa yekha m'nyumba yakeyake, osafika pamaso pa mfumu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu inati, Apatukire kunyumba ya iye yekha, koma asaone nkhope yanga. Chomwecho Abisalomu anapatukira kunyumba ya iye yekha, wosaona nkhope ya mfumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma mfumu inati, “Iye apite ku nyumba yake; asaone nkhope yanga.” Kotero Abisalomu anapita ku nyumba yake ndipo sanakumane ndi mfumu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu inati, Apambukire ku nyumba yaiye yekha, koma asaone nkhope yanga. Comweco Abisalomu anapambukira ku nyumba ya iye yekha, wosaona nkhope ya mfumu.