2 Samuel 14:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'dziko lonse la Israele panalibe munthu wina aliyense wokongola ndi wochititsa kaso ngati Abisalomu. Kuyambira kumapazi mpaka kumutu analibe chilema chilichonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo m'Israele monse munalibe wina anthu anamtama kwambiri chifukwa cha kukongola kwake monga Abisalomu; kuyambira ku mapazi kufikira pakati pa mutu wake mwa iye munalibe chilema.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼdziko lonse la Israeli munalibe munthu amene anayamikidwa chifukwa cha maonekedwe ake wokongola ngati Abisalomu. Kuyambira kumutu mpaka ku mapazi ake, analibe chilema.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo m'lsrayeli monse munalibe wina anthu anamtama kwambiri cifukwa ca kukongola kwace monga Abisalomu; kuyambira ku mapazi kufikira pakati pa mutu wace mwa iye munalibe cirema.