2 Samuel 14:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chaka chilichonse ankameta tsitsi lake, chifukwa linkamlemera kwambiri. Ankati akalimeta Abisalomuyo, naliyesa pa sikelo tsitsilo, linkalemera makilogramu aŵiri, potsata muyeso wa mfumu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pometa tsitsi lake amameta potsiriza chaka, chifukwa tsitsi linamlemerera, chifukwa chake atalimeta anayesa tsitsi la pa mutu wake, napeza masekeli mazana awiri, monga mwa muyeso wa mfumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi ina iliyonse akamameta tsitsi lake, ankameta pamene layamba kumulemera. Akatero amaliyeza, ndipo limalemera makilogalamu awiri pa sikelo yaufumu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pometa tsitsi lace amameta potsiriza caka, cifukwa tsitsi linamlemerera, cifukwa cace atalimeta anayesa tsitsi la pa mutu wace, napeza masekeli mazana awiri, monga mwa muyeso wa mfumu.