2 Samuel 14:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Yowabu adanyamuka kupita kunyumba kwa Abisalomu, nakamufunsa kuti, “Bwanji atumiki ako atentha munda wanga?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Yowabu ananyamuka nafika kwa Abisalomu kunyumba yake, nanena naye, Chifukwa ninji anyamata anu anatentha za m'munda mwanga;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Yowabu anapita ku nyumba ya Abisalomu ndipo anati kwa iye, “Nʼchifukwa chiyani antchito ako atentha munda wanga?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Yoabu ananyamuka nafika kwa Abisalomu ku nyumba yace, nanena naye, Cifukwa ninji anyamata anu anatentha za m'munda mwanga;