2 Samuel 14:32 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Abisalomu adayankha kuti, “Taona, ine ndinkatumiza mau kwa iwe kuti ndidzakutume kwa mfumu kukaifunsa kuti chifukwa chiyani ndidachoka ku Gesuri kubwera kuno? Kunali kwabwino koposa kuti ine ndizikhalabe konkuja.” Abisalomu adapitirira nati, “Ndipite basi kwa mfumu. Ngati ndili ndi cholakwa, mfumuyo ikandiphe.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Abisalomu nayankha Yowabu, Ona, ndinatumiza kwa iwe kuti, Bwera kuno kuti ndikutume kwa mfumu kukanena, Ine ndinabwereranji kuchokera ku Gesuri? Mwenzi nditakhala komweko; chifukwa chake tsono mundilole kuona nkhope ya mfumu; ndipo ngati mulinso mphulupulu mwa ine andiphe ndithu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abisalomu anati kwa Yowabu, “Taona, ine ndinatumiza mawu kwa iwe ndipo ndinati, ‘Bwera kuno kuti ndikutume kwa mfumu kukafunsa kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani ine ndinabwera kuchokera ku Gesuri? Zikanakhala bwino ndikanakhala komweko!’ Tsono pano ndikufuna kuonana ndi mfumu, ndipo ngati ndili olakwa mfumuyo indiphe.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Abisalomu nayankha Yoabu, Ona, ndinatumiza kwa iwe kuti, Bwera kuno kuti ndikutume kwa mfumu kukanena, Ine ndinabwereranji kucokera ku Gesuri? mwenzi nditakhala komweko; cifukwa cace tsono mundilole kuona nkhope ya mfumu; ndipo ngati mulinso mphulupulu mwa ine andiphe ndithu.