2 Samuel 14:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumuyo idamufunsa kuti, “Chikukuvutani nchiyani, mai?” Mkaziyo adayankha kuti, “Ha! Munthune ndine mkazi wamasiye. Mwamuna wanga adafa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumuyo inanena naye, Usowanji? Iye nayankha, Zoonadi ine ndine mkazi wamasiye, mwamuna wanga anamwalira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu inamufunsa kuti, “Kodi chikukusautsa iwe nʼchiyani?” Iye anayankha kuti, “Ine ndine mkazi wamasiye, mwamuna wanga anamwalira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumuyo inanena naye, Usowanji? iye nayankha, Zoonadi ine ndine mkazi wamasiye, mwamuna wanga ana mwalira.