2 Samuel 14:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye ine mdzakazi wanu ndinali ndi ana aamuna aŵiri, anawo ankamenyana kuminda. Panalibe wina aliyense woti aŵaleretse, choncho wina adakantha mnzake mpaka kumupha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mdzakazi wanu ndinali nao ana amuna awiri, ndipo awiriwo analimbana kumunda, panalibe wina wakuwaletsa, koma wina anakantha mnzake namupha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine wantchito wanu ndinali ndi ana aamuna awiri. Iwo anayamba kumenyana mʼmunda, ndipo panalibe woti awaleretse. Wina anakantha mnzakeyo mpaka kumupha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mdzakazi wanu ndinali nao ana amuna awiri, ndipo awiriwa analimbana kumunda, panaboo wina wakuwaletsa, koma wina anakantha mnzace namupha.