2 Samuel 14:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono banja lonse landiwukira ine mdzakazi wanu, akunena kuti, ‘Utipatse mwana wako amene adapha mbale wake, kuti ife timuphe chifukwa cha mbale wake amene iye adaphayo.’ Motero anthuwo adzaononganso mloŵachuma. Anthuwo adzapha mwana wanga amene wanditsalira, ndipo dzina la mwamuna wanga silidzakumbukika, pakuti sipadzakhalanso mwana pa banja lathu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo onani, chibale chonse chinaukira mdzakazi wanu, ndi kuti, Upereke iye amene anakantha mbale wake, kuti timuphe chifukwa cha moyo wa mbale wake amene anamupha; koma pakutero adzaononga wolowa yemwe; chomwecho adzazima khala langa lotsala, ndipo sadzasiyira mwamuna wanga dzina kapena mbeu kunja kuno.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono banja lonse landiwukira ine, wantchito wanu. Iwo akuti, ‘Utipatse mwana amene anakantha mʼbale wakeyo kuti timuphe chifukwa cha moyo wa mʼbale wake amene anaphedwayo. Ife tidzaphanso mlowamʼmalo.’ Anthuwo adzapha mwana wanga amene wanditsalira, ndipo dzina la mwamuna wanga silidzakumbukika pakuti sipadzakhalanso mwana pa banja lathu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo onani, cibale conse cinaukira mdzakazi wanu, ndi kuti, Upereke iye amene anakantha mbale wace, kuti timuphe cifukwa ca moyo wa mbale wace amene anamupha; koma pakutero adzaononga wolowa yemwe; comweco adzazima khara langa lotsala, ndipo sadzasiyira mwamuna wanga dzina kapena mbeu kunja kuno.