2 Samuel 14:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mkazi wa ku Tekowa uja adauza mfumu kuti, “Inu amfumu, mlandu umenewu ugwere ine ndi banja la bambo wanga, inuyo mukhale osalakwa pamodzi ndi banja lanu lonse.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mkazi wa ku Tekowayo ananena ndi mfumu, Mbuye wanga mfumu, mphulupulu ikhale pa ine ndi pa nyumba ya atate wanga; ndipo mfumu ndi mpando wachifumu wao zikhale zopanda chifukwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma mkazi wochokera ku Tekowayo anati kwa mfumu, “Mbuye wanga mfumu, kulakwa kukhale pa ine ndi banja la abambo anga ndipo mfumu ndi mpando wanu waufumu mukhale osalakwa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mkazi wa ku Tekowayo ananena ndi mfumu, Mbuye wanga mfumu, mphulupulu ikhale pa ine ndi pa nyumba ya atate wanga; ndipo mfumu ndi mpando wacifumu wao zikhale zopanda cifukwa.