2 Samuel 15:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Abisalomu popita, adatenga anthu okwanira 200 a ku Yerusalemu. Iwoŵa anali alendo oitanidwa chabe, mwakuti ankangopita osadziŵa chilichonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamodzi ndi Abisalomu panapita anthu mazana awiri a ku Yerusalemu ndiwo oitanidwa, namuka m'kupulukira kwao, osadziwa kanthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu 200 ochokera mu Yerusalemu anapita naye Abisalomu. Iwo anayitanidwa monga alendo ndipo anapita osadziwa chilichonse pa nkhaniyi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamodzi ndi Abisalomu panapita anthu mazana awiri a ku Yerusalemu ndiwo oitanidwa, namuka m'kupulukira kwao, osadziwa kanthu.