2 Samuel 15:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene Abisalomu ankapereka nsembe ku Hebroni, adatumiza mau kukaitana Ahitofele, mlangizi wa Davide wa ku mzinda wa Gilo. Motero chiwembucho chidakula kwambiri. Nawonso anthu otsatira Abisalomu adanka nachulukirachulukira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Abisalomu anaitana Ahitofele Mgiloni, mphungu wa Davide, kumudzi wake ndiwo Gilo, pamene iye analikupereka nsembe. Ndipo chiwembucho chinali cholimba; pakuti anthu anachulukachulukabe kwa Abisalomu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene Abisalomu amapereka nsembe, iye anayitanitsanso Ahitofele Mgiloni, mlangizi wa Davide, wa ku Gilo, kotero kuwukiraku kunakula kwambiri, ndipo anthu otsatira Abisalomu anapitirira kuchuluka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Abisalomu anaitana Ahitofeli Mgiloni, mphungu wa Davide, ku mudzi wace ndiwo Gilo, pamene iye analikupereka nsembe. Ndipo ciwembuco cinali colimba; pakuti anthu anacurukacurukabe kwa Abisalomu.