2 Samuel 15:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye Davide adauza ankhondo ake amene anali naye ku Yerusalemu kuti, “Nyamukani, tiyeni tithaŵe kuti tingasoŵe mpata wothaŵira Abisalomu. Fulumirani, kuti angatipeze mwamsanga, ndipo angatithire nkhondo ndi kutipha tonse mumzinda muno.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide ananena nao anyamata ake onse akukhala naye ku Yerusalemu, Nyamukani tithawe, tikapanda kuthawa palibe mmodzi wa ife adzapulumuka Abisalomu; fulumirani kuchoka, angatipeze msanga ndi kutigwetsera zoipa ndi kukantha mudzi ndi lupanga lakuthwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Davide anati kwa akuluakulu ake amene anali mu Yerusalemu. “Bwerani! Tiyeni tithawe, mwina palibe adzapulumuke kwa Abisalomu. Tiyeni tichoke msanga, mwina iye adzabwera msanga ndi kutipitirira, nʼkuwononga ife ndi mzinda wathu ndi lupanga.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide ananena nao anyamata ace onse akukhala naye ku Yerusalemu, Nyamukani tithawe, tikapanda kuthawa palibe mmodzi wa ife adzapulumuka Abisalomu; fulumirani kucoka, angatipeze msanga ndi kutigwetsera zoipa ndi kukantha mudzi ndi lupanga lakuthwa.