2 Samuel 15:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho mfumu idatuluka, nipita pamodzi ndi anthu onse a pabanja pake. Koma mfumuyo idasiya azikazi ake khumi kuti azisunga mudzi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mfumu nituluka, ndi banja lake lonse linamtsata. Ndipo mfumu inasiya akazi khumi ndiwo akazi aang'ono, kusunga nyumbayo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu inanyamuka pamodzi ndi banja lake lonse. Koma iye anasiya azikazi khumi kuti azisamalira nyumba yaufumu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mfumu nituruka, ndi banja lace lonse tinamtsata. Ndipo mfumu inasiya akazi khumi ndiwo akazi ang'ono, kusunga nyumbayo.