2 Samuel 15:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene mfumu idatuluka, anthu onse adaitsata. Onsewo adakaima pa nyumba yomalizira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu inatuluka, ndi anthu onse anamtsata; naima kunyumba ya pa yokha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kotero mfumu inanyamuka pamodzi ndi anthu onse oyitsatira, ndipo anayima pamalo pena chapatalipo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu inaturuka, ndi anthu onse anamtsata; naima ku nyumba ya payokha.