2 Samuel 15:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zitatero, mfumu idafunsa Itai Mgiti kuti, “Chifukwa chiyani ukupita nafe pamodzi? Bwerera, ukakhale ndi mfumu ija. Paja iwe ndiwe mlendo, ndiponso ndiwe munthu wothaŵa kwanu, motero bwerera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pomwepo mfumu inanena kwa Itai Mgiti, Bwanji ulikupita nafe iwenso? Ubwerere nukhale ndi mfumu; pakuti uli mlendo ndi wopirikitsidwa; bwerera ku malo a iwe wekha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu inati kwa Itai Mgiti, “Nʼchifukwa chiyani iwe ukupita ndi ife? Bwerera ndipo ukakhale ndi mfumu Abisalomu. Iwe ndiwe mlendo munthu wothawa kwawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pomwepo mfumu inanena kwa Itai Mgiti, Bwanji ulikupita nafe iwenso? Ubwerere nukhale ndi mfumu; pakuti uli mlendo ndi wopitikitsidwa; bwerera ku malo a iwe wekha.