2 Samuel 15:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Abisalomu ankadzuka m'mamaŵa, namaima pa njira ya ku chipata cha mzinda. Munthu wina aliyense akakhala ndi mlandu kuti apite kwa mfumu kukaweruzidwa, Abisalomu ankamuitana, namufunsa kuti, “Ukuchokera ku mzinda uti?” Akayankha kuti, “Mtumiki wanune, ndine wa fuko lakutilakuti, m'dziko la Israele,”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Abisalomu analawirira, nakaima pa njira ya kuchipata; ndipo kunatero, pakakhala munthu aliyense ndi mlandu woyenera kufika kwa mfumu kuti aweruze, Abisalomu anamuitana, nati, Ndinu wa kumudzi uti? Ndipo anati, Mnyamata wanu ndiye wa fuko lina la Aisraele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye amadzuka mmamawa ndi kuyima pa njira yopita ku chipata cha mzinda. Munthu wina aliyense akakhala ndi zodandaula zopita nazo kwa mfumu kuti akaweruze, Abisalomu amamuyitana iye ndi kumufunsa kuti, “Kodi ukuchokera ku limodzi mwa mafuko a Israeli?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Abisalomu analawirira, nakaima pa njira ya kucipata; ndipo kunatero, pakakhala munthu ali yense ndi mrandu woyenera kufika kwa mfumu kuti aweruze, Abisalomu anamuitana, nati, Ndinu wa ku mudzi uti? Ndipo anati, Mnyamata wanu; ndiye wa pfuko tina la Aisrayeli.