2 Samuel 15:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwe wangobwera dzulo. Ndiye ine ndikutenge lero, kuti uzinka nuyenda nane? Ine ndemwe sindikudziŵa kumene ndikupita. Bwerera ndi anthu akwanu, ndipo Chauta akukomere mtima ndi kukuchitira zabwino mwa kukhulupirika kwake.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Popeza unangofika dzulo lokha, kodi ndidzakutenga lero kuyendayenda nafe popeza ndipita pomwe ndiona popita? Ubwerere nubwereretsenso abale ako; chifundo ndi zoonadi zikhale nawe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wangobwera dzulo lomweli, lero ndikutenge kuti uziyendayenda ndi ife, pamene ine sindikudziwa kumene ndikupita? Bwerera, ndipo tenga abale ako. Chifundo ndi kukhulupirika zikhale nawe.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Popeza unangofika dzulo lokha, kodi ndidzakutenga lero kuyendayenda nafe popeza ndipita pomwe ndiona popita? ubwerere nubwereretsenso abale ako; cifundo ndi zoonadi zikhale nawe.