2 Samuel 15:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Itai adayankha mfumu kuti, “Pali Chauta wamoyo, ndiponso pali inu nomwe mbuyanga mfumu, kulikonse kumene inu mbuyanga mfumu mudzakhale, kaya mpa imfa kaya mpa moyo, ine mtumiki wanu ndidzakhalanso komweko.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Itai nayankha mfumu nuti, Pali Yehova, pali mbuye wanga mfumu, zoonadi apo padzakhala mbuye wanga mfumu, kapena mpa imfa kapena mpa moyo, pomwepo padzakhalanso mnyamata wanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Itai anayankha mfumu kuti, “Pali Yehova wamoyo, kulikonse kumene mbuye wanga mfumu mudzakhala, kaya ndi moyo kapena imfa, mtumiki wanu adzakhala komweko.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Itai nayankha mfumu nuti, Pali Yehova, pali mbuye wanga mfumu, zoonadi apo padzakhala mbuye wanga mfumu, kapena mpa imfa kapena mpa moyo, pomwepo padzakhalanso mnyamata wanu.