2 Samuel 15:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Davide adauza Itai kuti, “Chabwino, tiye.” Motero Itai Mgiti uja adaoloka mtsinje wa Kidroni, pamodzi ndi anthu ake, akuluakulu ndi ang'onoang'ono omwe amene anali naye.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide ananena ndi Itai, Tiye nuoloke. Ndipo Itai Mgiti anaoloka, ndi anthu ake onse, ndi ana ang'ono onse amene anali naye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide anati kwa Itai, “Tiye pita nafe” Kotero Itai Mgiti anayenda pamodzi ndi anthu ake ndi mabanja amene anali naye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide ananena ndi Itai, Tiye nuoloke. Ndipo Itai Mgiti anaoloka, ndi anthu ace onse, ndi ana ang'ono onse amene anali naye.