2 Samuel 15:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono anthu onse adayamba kulira mofuula pamene mfumu ndi otsatira ake ankapita. Choncho mfumuyo idaoloka mtsinjewo, ndipo anthu onse adamtsatira kupita ku chipululu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo dziko lonse linalira ndi mau okweza; ndipo anthu onse anaoloka, ndi mfumu yomwe inaoloka mtsinje wa Kidroni, ndipo anthu onse anaolokera ku njira ya kuchipululu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu onse a madera ozungulira analira mofuwula pamene anthu onsewo amadutsa. Mfumunso inawoloka chigwa cha Kidroni, ndipo anthu onse anayenda kulowera ku chipululu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo dziko lonse linalira ndi mau okweza; ndipo anthu onse anaoloka, ndi mfumu yomwe inaoloka mtsinje wa Kidroni, ndipo anthu onse anaolokera ku njira ya kucipululu.