2 Samuel 15:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ansembe, Abiyatara ndi Zadoki adapita nao pamodzi ndi Alevi onse, atanyamula Bokosi lachipangano la Chauta. Adatula pansi Bokosilo, mpaka anthu onse atatuluka mumzindamo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo onani, Zadoki yemwe anadza, ndi Alevi onse pamodzi naye, alikunyamula likasa la chipangano la Mulungu; natula likasa la Mulungu; ndi Abiyatara anakwera kufikira anthu onse anatha kutuluka m'mudzimo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zadoki anali nawonso, ndipo Alevi onse amene anali naye ananyamula Bokosi la Chipangano la Mulungu. Iwo anayika pansi Bokosi la Mulungulo ndipo Abiatara ankapereka nsembe mpaka pamene anthu onse anamaliza kutuluka mu mzinda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo onani, Zadoki yemwe anadza, ndi Alevi onse pamodzi naye, alikunyamula likasa la cipangano la Mulungu; natula likasa la Mulungu; ndi Abyatara anakwera kufikira anthu onse anatha kuturuka m'mudzimo.