2 Samuel 15:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo mfumu idauza Zadoki kuti, “Nyamulani Bokosi lachipangano la Chautali, mubwerere nalo mu mzinda. Chauta akandikomera mtima, adzandibweza kuti ndidzaliwonenso Bokosilo pamodzi ndi malo ake omwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu inanena ndi Zadoki, Ubwerera nalo likasa la Mulungu kumudziko; akandikomera mtima Yehova, Iye adzandibwezanso, nadzandionetsanso ili, ndi pokhala pake pomwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka mfumu inati kwa Zadoki, “Tenga Bokosi la Mulungu ubwerere nalo mu mzinda. Ngati ndidzapeza chifundo pamaso pa Yehova, adzandibweretsa kuti ndilionenso ndi malo ake okhalamo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu inanena ndi Zadoki, Ubwererenalo likasa la Mulungu kumudziko; akandikomera mtima Yehova, iye adzandibwezanso, nadzandionetsanso gi, ndi pokhala pace pomwe.