2 Samuel 15:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo mfumuyo idauzanso Zadoki wansembe uja kuti, “Bwerera ku mzinda mwamtendere, iwe pamodzi ndi Abiyatara, ndi ana anu aŵiri, mwana wako Ahimaazi ndi Yonatani mwana wa Abiyatara.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu inanenanso ndi Zadoki wansembeyo, Suli mlauli kodi? Ubwere kumudzi mumtendere pamodzi ndi ana ako amuna awiri, Ahimaazi mwana wako ndi Yonatani mwana wa Abiyatara.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu inatinso kwa wansembe Zadoki, “Kodi siwe mlosi? Bwerera mu mzinda mwamtendere pamodzi ndi mwana wako Ahimaazi ndi Yonatani mwana wa Abiatara. Iwe ndi Abiatara tengani ana anu awiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu inanenanso ndi Zadoki wansembeyo, Suli mlauli kodi? ubwere kumudzi mumtendere pamodzi ndi ana ako amuna awiri, Ahimaazi mwana wako ndi Jonatani mwana wa Abyatara.