2 Samuel 15:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Abisalomu ankamuuza kuti, “Taona, zimene ukunenazi nzabwino ndi zolungama. Koma mfumu sidaike munthu woti azimva madandaulo anu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Abisalomu nanena naye, Ona zokamba zako ndizo zabwino ndi zolungama; koma mfumu sinauze wina kuti adzamve za iwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Abisalomu amanena kwa iye kuti, “Taona, madandawulo ako ndi abwino ndi oyenera, koma palibe woyimira mfumu woti akumvere.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Abisalomu nanena naye, Ona zokamba zako ndizo zabwino ndi zolungama; koma mfumu sinauze wina kuti adzamve za iwe.