2 Samuel 15:30 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Davide adakwera phiri la Olivi, akunka nalira, osavala kanthu kuphazi, atafundira kumutu. Anthu onse amene anali naye adafundanso kumutu, ndipo nawonso adakwera phiri akunka nalira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide anakwera pa chikweza cha ku Azitona nakwera nalira misozi; ndipo anafunda mutu wake nayenda ndi mapazi osavala; ndi anthu onse amene anali naye anafunda munthu yense mutu wake ndipo anakwera, nalira misozi pokwerapo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Davide anapitirira ndi kukakwera phiri la Olivi akupita nalira. Anafunda kumutu koma sanavale nsapato. Anthu onse amene anali naye anafundanso kumutu, ndipo nawonso amalira pamene amapita.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide anakwera pa cikweza ca ku Azitona nakwera nalira misozi; ndipo anapfunda mutu wace nayenda ndi mapazi osabvala; ndi anthu onse amene anali naye anapfunda munthu yense mutu wace, ndipo anakwera, nalira misozi pokwerapo.