2 Samuel 15:31 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka Davide adamva kuti Ahitofele ali pakati pa anthu ogalukira, pamodzi ndi Abisalomu. Tsono Davideyo adayamba kupemphera, adati, “Ine Chauta ndikukupemphani, musandutse uphungu wa Ahitofele kuti ukhale uchitsiru.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo wina anauza Davide nati, Ahitofele ali pakati pa opangana chiwembu pamodzi ndi Abisalomu. Davide nati, Yehova, musandulize uphungu wa Ahitofele ukhale wopusa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Davide anamva kuti, “Ahitofele ali pakati pa anthu owukira pamodzi ndi Abisalomu.” Choncho Davide anapemphera, “Inu Yehova, musandutse uphungu wa Ahitofele ukhale uchitsiru.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo wina anauza Davide nati, Ahitofeli ali pakati pa opangana ciwembu pamodzi ndi Abisalomu. Davide nati, Yehova, musandulize uphungu wa Ahitofeli ukhale wopusa.