2 Samuel 15:32 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Davide atafika pamwamba pa phiri pomwe ankapembedzerapo Mulungu, Husai Mwariki adadzakumana naye atang'amba mwinjiro ndi kudzithira dothi kumutu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali pakufika Davide ku mutu wa phiri, kumene amapembedza Mulungu, onani, Husai Mwariki anadzakomana naye ali ndi malaya ake ong'ambika, ndi dothi pamutu pake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide atafika pamwamba pa phiri pomwe anthu ankapembedzerapo Mulungu, Husai Mwariki anadzakumana naye atangʼamba mkanjo wake ndi kudzithira fumbi kumutu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali pakufika Davide ku mutu wa phiri, kumene amapembedza Mulungu, onani, Husai M-ariki anadzakomana naye ali ndi maraya ace ong'ambika, ndi dothi pamutu pace.