2 Samuel 15:34 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma makamaka iwe ubwerere ku mzinda, ukamuuze Abisalomu kuti, ‘Inu amfumu, ine ndidzakhala mtumiki wanu. Monga kale ndinali mtumiki wa bambo wanu, momwemonso tsopano ndidzakhala mtumiki wanu.’ Ukakatero ukandigonjetsera uphungu wa Ahitofele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma ukabwerera kumudzi, ndi kunena ndi Abisalomu, Ine ndine mnyamata wanu, mfumu; monga kale ndinali mnyamata wa atate wanu, momwemo tsopano ndidzakhala mnyamata wanu; pomwepo udzanditsutsira uphungu wa Ahitofele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ngati ubwerera ku mzinda ndi kukanena kwa Abisalomu kuti, ‘Inu mfumu ine ndidzakhala wantchito wanu.’ Mʼmbuyomu ndinali wantchito wa abambo anu koma tsopano ndidzakhala wantchito wanu. Ukatero udzandithandiza kulepheretsa malangizo a Ahitofele.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma ukabwerera kumudzi, ndi kunena ndi Abisalomu, Ine ndine mnyamata wanu, mfumu; monga kale ndinali mnyamata wa atate wanu, momwemo tsopano ndidzakhala mnyamata wanu; pomwepo udzanditsutsira uphungu wa Ahitofeli.