2 Samuel 15:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo ankapitirira kunena kuti, “Achikhala adaaika ine, kuti ndikhale woweruza m'dziko muno! Bwenzi munthu aliyense amene ali ndi mlandu, kapena vuto lina lililonse, atabwera kwa ine, ndipo ine ndikadamuweruza molungama munthuyo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Abisalomu anatinso, Mwenzi atandiika ine ndikhale woweruza m'dzikomo, kuti munthu yense amene ali ndi mlandu wake kapena chifukwa chake, akadafika kwa ine; ndipo ndikadamchitira zachilungamo!
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Abisalomu amawonjezera kunena kuti, “Ine ndikanangosankhidwa kukhala woweruza mʼdziko muno bwenzi munthu aliyense amene ali ndi madandawulo kapena milandu akubwera kwa ine ndipo ndikanaonetsetsa kuti chilungamo chachitika.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Abisalomu anatinso, Mwenzi atandiika ine ndikhale woweruza m'dzikomo, kuti munthu yense amene ali ndi mrandu wace kapena cifukwa cace, akadafika kwa ine; ndipo ndikadamcitira zacilungamo!