2 Samuel 15:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Umu ndimo m'mene Abisalomu ankachitira ndi Aisraele onse amene ankabwera kwa mfumu kuti akaweruzidwe. Motero Abisalomu adaŵagwira mitima Aisraele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Abisalomu anachitira zotero Aisraele onse akudza kwa mfumu kuti aweruze mlandu wao; chomwecho Abisalomu anakopa mitima ya anthu a Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abisalomu amachitira izi Aisraeli onse amene amabwera kwa mfumu kuti adzaweruzidwe ndipo Abisalomuyo anagwira mtima anthu a mu Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Abisalomu anacitira zotero Aisrayeli onse akudza kwa mfumu kuti aweruze mrandu wao; comweco Abisalomu anakopa mitima ya anthu a Israyeli.