2 Samuel 16:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Davide atabzola pang'ono pamwamba pa phiri, adakumana ndi Ziba, mtumiki wa Mefiboseti, ali ndi abulu a chishalo pa msana, atasenza buledi wokwanira 200, masangwe a mphesa 100, zipatso zapachilimwe 100, ndiponso thumba la vinyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene Davide anapitirira pang'ono pamutu pa phiri, onani, Ziba mnyamata wa Mefiboseti anakomana naye, ali nao abulu awiri omanga mbereko, ndi pamenepo mitanda ya mikate mazana awiri, ndi nchinchi zamphesa zana limodzi, ndi zipatso za m'dzinja zana limodzi, ndi thumba la vinyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide atapitirira pangʼono pamwamba pa phiri, anakumana ndi Ziba mtumiki wa Mefiboseti akudikira kuti akumane naye. Iye anali ndi abulu a chishalo pa msana ndipo ananyamula malofu a buledi 200, ntchintchi 100 za mphesa zowuma, zipatso za pa nthawi yachilimwe 100 ndi thumba la vinyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene Davide anapitirira pang'ono pamutu pa phiri, onani, Ziba mnyamata wa Mefiboseti anakomana naye, ali nao aburu awiri omanga mbereko, ndi pamenepo mitanda ya mikate mazana awiri, ndi ncinci zamphesa zana limodzi, ndi zipatso za m'dzinja zana limodzi, ndi thumba la vinyo.