2 Samuel 16:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma mfumu idayankha kuti, “Zikukukhudzani bwanji zimenezi, inu ana a Zeruya? Ngati iyeyu akunditukwana chifukwa choti Chauta wachita kumuuza kuti, ‘Mtukwane Davideyu’, ndani angamufunse kuti, ‘Bwanji wachita zimenezi?’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mfumu niti, Ndili ndi chiyani ndi inu, ana a Zeruya? Pakuti atukwana, ndi pakuti Yehova ananena naye, Utukwane Davide; ndani tsono adzanena, Watero chifukwa ninji?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma mfumu inati, “Inu ana a Zeruya, kodi ndikuchitireni chiyani? Ngati iye akutukwana chifukwa Yehova wamuwuza kuti, ‘Tukwana Davide,’ angafunse ndani kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani ukuchita zimenezi?’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mfumu niti, Ndiri ndi ciani ndi inu, ana a Zeruya? Pakuti atukwana, ndi pakuti Yehova ananena naye, Utukwane Davide; ndani tsono adzanena, Watero cifukwa ninji?