2 Samuel 16:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Davide adauza Abisai ndi atsogoleri ake kuti, ‘Mwana wanga weniweni akufuna kundipha, nanga nanji Mbenjaminiyu? Mlekeni azitukwana, pakuti wachita kumlamula ndi Chauta kuti atero.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide ananena ndi Abisai ndi anyamata ake onse, Onani, mwana wanga wotuluka m'matumbo anga, alikufuna moyo wanga; koposa kotani nanga Mbenjamini uyu? Mlekeni, atukwane, pakuti Yehova anamuuza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Davide anati kwa Abisai ndi akuluakulu ake onse, “Mwana wanga wobereka ndekha akufuna kundipha. Nanji tsono munthu wa fuko la Benjamini uyu! Musiyeni; mulekeni atukwane pakuti Yehova wachita kumuwuza kuti atero.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide ananena ndi Abisai ndi anyamata ace onse, Onani, mwana wanga woturuka m'matumbo anga, alikufuna moyo wanga; koposa kotani nanga Mbenjamini uyu? mlekeni, atukwane, pakuti Yehova anamuuza.