2 Samuel 16:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Abisalomu adafunsa Husai kuti, “Kodi ndimo m'mene umamkondera bwenzi lako? Chifukwa chiyani sudapite naye limodzi bwenzi lakoyo?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Abisalomu ananena ndi Husai, Kodi chimenechi ndi chifundo chako cha pa bwenzi lako? Unalekeranji kupita ndi bwenzi lako?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abisalomu anafunsa Husai, “Kodi ichi ndi chikondi chimene ukumuonetsa bwenzi lako? Nʼchifukwa chiyani sunapite ndi bwenzi lako?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Abisalomu ananena ndi Husai, Kodi cimeneci ndi cifundo cako ca pa bwenzi lako? unalekeranji kupita ndi bwenzi lako?