2 Samuel 16:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumu idafunsa Ziba kuti, “Chifukwa chiyani wabwera ndi zimenezi?” Ziba adayankha kuti, “Amfumu, abuluŵa ndi oti anthu a m'banja mwanu azikwerapo. Bulediyu, ndi zipatso zapachilimwezi nzoti ankhondo azidya, ndipo thumba la vinyoli nloti anthu amene azikomoka m'chipululu azimwa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu inanena ndi Ziba, Ulikutani ndi zimenezi? Nati Ziba, Abuluwo ndiwo kuti akaberekepo a pa banja lanu; ndi mitanda ya mikate ndi zipatso za m'dzinja ndizo zakudya za anyamata; ndi vinyoyo akufooka m'chipululu akamweko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu inafunsa Ziba kuti, “Nʼchifukwa chiyani wabweretsa izi?” Ziba anayankha kuti, “Abuluwa ndi oti anthu a mʼbanja mwanu akwerepo, buledi ndi zipatso ndi za anthu anu kuti adye, ndipo vinyoyo ndi woti atsitsimutse anthu amene atope mʼchipululu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu inanena ndi Ziba, Ulikutani ndi zimenezi? Nati Ziba, Aburuwo ndiwo kuti akaberekepo a pa banja lanu; ndi mitanda ya mikate ndi zipatso za m'dzinja ndizo zakudya za anyamata; ndi vinyoyo akufoka m'cipululu akamweko.