2 Samuel 16:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ahitofele adauza Abisalomu kuti, “Pitani mukaloŵe kwa azikazi a bambo wanu amene adaŵasiya kuti azisunga mudzi. Aisraele onse akadziŵa kuti bambo wanu akuipidwa nanu, onse amene akukutsataniŵa adzalimba mtima.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Ahitofele ananena ndi Abisalomu, Mulowe kwa akazi aang'ono a atate wanu amene iye anawasiya kuti asunge nyumbayo; ndipo Aisraele onse adzamva kuti atate wanu aipidwa nanu; pomwepo manja a onse akukhala nanu adzalimba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ahitofele anayankha kuti, “Mugone ndi azikazi a abambo anu amene awasiya kuti asamalire nyumba yaufumu. Aisraeli onse adzamva kuti mwachitira abambo anu chinthu chonyansa kotheratu ndipo anthu onse amene ali ndi iwe adzalimbikitsidwa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Ahitofeli ananena ndi Abisalomu, Mulowe kwa akazi ang'ono a atate wanu amene iye anawasiya kuti asunge nyumbayo; ndipo Aisrayeli onse adzamva kuti atate wanu aipidwa nanu; pomwepo manja a onse akukhala nanu adzalimba.