2 Samuel 16:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono masiku amenewo, malangizo amene ankapereka Ahitofele anali ngati mau ochokera kwa Mulungu. Choncho uphungu wonse wa Ahitofele ankaulemekeza Davide ndi Abisalomu yemwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo uphungu wa Ahitofele anaupangira masiku aja, unali monga ngati munthu anafunsira mau kwa Mulungu; uphungu wonse wa Ahitofele unali wotere kwa Davide ndi kwa Abisalomu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono masiku amenewo malangizo amene Ahitofele amapereka anali ngati mawu ochokera kwa Mulungu. Umu ndi mmene Davide ndi Abisalomu amalandirira malangizo onse a Ahitofele.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo uphungu wa Ahitofeli anaupangira masiku aja, unali monga ngati munthu anafunsira mau kwa Mulungu; uphungu wonse wa Ahitofeli unali wotere kwa Davide ndi kwa Abisalomu yemwe.