2 Samuel 16:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka mfumu idamufunsa kuti, “Nanga mwana wa mbuyako ali kuti?” Ziba adayankha kuti, “Watsalira ku Yerusalemu, poti akunena kuti, ‘Aisraele andibwezera ufumu wa bambo wanga tsopano.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu inati, Mwana wa mbuye wako ali kuti? Ziba nanena ndi mfumu, Onani, akhala ku Yerusalemu; pakuti anati, Lero nyumba ya Israele idzandibwezera ufumu wa atate wanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka mfumu inafunsa kuti, “Kodi chidzukulu cha mbuye wako chili kuti?” Ziba anati kwa iye, “Watsalira ku Yerusalemu chifukwa akuganiza kuti, ‘Lero Aisraeli andibwezera ufumu wa agogo anga.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu inati, Mwana wa mbuye wako ali kuti? Ziba nanena ndi mfumu, Onani, akhala ku Yerusalemu; pakuti anati, Lero nyumba ya Israyeli idzandibwezera ufumu wa atate wanga.