2 Samuel 16:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene mfumu Davide adafika ku mzinda wa Bahurimu, kudatulukira munthu wa ku banja la Saulo, dzina lake Simei, mwana wa Gera. Ankabwera akungotukwana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pakufika mfumu Davide ku Bahurimu, onani, panatuluka pamenepo munthu wa banja la nyumba ya Saulo, dzina lake ndiye Simei, mwana wa Gera; iyeyu anatulukako, nayenda natukwana.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu Davide itayandikira Bahurimu, munthu wochokera ku fuko limodzi ndi banja la Sauli anabwera kuchokera mʼmenemo. Dzina lake linali Simei, mwana wa Gera ndipo amatukwana pamene amabwera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pakufika mfumu Davide ku Bahurimu, onani, panaturuka pamenepo munthu wa banja la nyumba ya Sauli, dzina lace ndiye Simeyi, mwana wa Gera; iyeyu anaturukako, nayenda natukwana.