2 Samuel 16:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Simeiyo ankaponya miyala mfumu Davide ndiponso nduna zake zonse. Nthaŵiyo nkuti atetezi ake ndi ankhondo ake ali kwete kuzungulira mfumuyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iye anaponya miyala Davide ndi anyamata onse a mfumu Davide, angakhale anthu onse ndi ngwazi zonse zinali ku dzanja lamanja ndi ku dzanja lamanzere kwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye amagenda Davide miyala ndi akuluakulu onse a mfumu, ngakhale kuti ankhondo onse ndi oteteza Davide anali ali kumanzere ndi kumanja kwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye anaponya miyala Davide ndi anyamata onse a mfumu Davide, angakhale anthu onse ndi ngwazi zonse zinali kudzanja lamanja ndi ku dzanja lamanzere kwace.